Mawu a M'munsi
c Anthu ophunzira amatsutsana pa nkhani ya kumene kunachokera dzinali. M’Chihebri dzina lakuti Mose limatanthauza “Wochotsedwa M’madzi; Wopulumutsidwa M’madzi.” Flavius Josephus, yemwe ndi katswiri wa mbiri yakale anati dzina lakuti Mose linachokera ku mawu aŵiri a chinenero cha ku Aigupto otanthauza kuti “madzi” ndiponso “pulumuka.” Masiku ano, anthu ena ophunzira amakhulupiriranso kuti dzinali n’lochokera ku Aigupto koma mmene iwowo amaonera, tanthauzo la dzinali liyenera kukhala lakuti “Mwana Wamwamuna.” Komabe iwoŵa amatero chifukwa choti dzina lakuti “Mose” limamveka mofanana ndi maina ena a ku Aigupto. Popeza kuti palibe amene amadziŵa mmene chinenero chakale cha Ahebri ndi cha Aigupto chinkatchulidwira, mfundo zoterezi n’zongoganizira chabe basi.