Mawu a M'munsi
d Buku lakuti Israel in Egypt limati: “Zakuti Mose analeredwera m’nyumba yachifumu ya Aaigupto zimamveka ngati nthano chabe. Komano mukaonetsetsa mmene zinthu zinkayendera m’nyumba yachifumu ku Aigupto m’zaka za m’ma 1550 mpaka 1070 Nyengo Yathu Ino Isanakwane mungathe kuona kuti sinthano chabe ayi. Thutmose Wachitatu . . . anayambitsa zomatenga akalonga ogwidwa pankhondo ochokera m’mayiko a kumadzulo kwa Asia n’kuwapititsa ku Aiguptoko kuti awaphunzitse moyo wa Aaigupto . . . Motero, sizinali zachilendo kuona akalonga aamuna ndiponso aakazi ochokera kunja ali m’nyumba yachifumu ya ku Aigupto.”