Mawu a M'munsi
a Mukangoyamba kumene kusamba, mukhoza kumasamba mwina kaŵiri kapena kuposa pamenepo pamwezi, kapena mukhoza kumadumpha miyezi ina osasamba. Magazi amene amatuluka akhoza kukhala ochuluka mosiyanasiyananso. Zonsezi siziyenera kukuopsani. Komabe, kusamba mosakhazikika bwino kwa chaka chimodzi kapena ziŵiri kukhoza kusonyeza kuti muyenera kukaonana ndi dokotala.