Mawu a M'munsi
a Zina mwa zinthu zimene zimachititsa azimayi kukhala osabereka ndi kusagwira bwino ntchito kwa ziwalo zimene zimapanga mazira, kutsekeka kwa njira zopita ku chiberekero, kapena matenda a m’chiberekero. Nthaŵi zambiri amuna amakhala osabereka chifukwa chakuti thupi lawo silipanga ubwamuna wokwanira kapena silipanga n’komwe ubwamunawo.