Mawu a M'munsi
a Nkhani yakuti, “Achinyamata Akufunsa Kuti . . . Kodi Mnyamata Ndingamuuze Bwanji Kuti Ndikumufuna?” (November 8, 2004) inafotokoza kuti m’mayiko ena zingakhale zosemphana ndi chikhalidwe chawo kuti mkazi auze mwamuna kuti akumufuna chibwenzi. Ngakhale kuti Baibulo sililetsa akazi kufunsira amuna, limalimbikitsa Akristu kupewa kukhumudwitsa anthu ena. Choncho atsikana amene akufuna kuti Mulungu awadalitse afunika kuganizira malangizo a m’Baibulo akamaganizira zoti achite pa nkhani imeneyi.—Mateyu 18:6; Aroma 14:13; 1 Akorinto 8:13.