Mawu a M'munsi
a Buku lomwelo linati mosiyana ndi wachinyamata amene amasungulumwa nthawi zina, achinyamata ena amakhala osungulumwa nthawi zambiri ndiponso kwa nthawi yaitali. Wachinyamata woteroyo “amakhulupirira kuti adzakhala wopanda mnzake mpaka kalekale, kuti palibe chomwe angachite kuti asinthe zimenezo, ndiponso kuti zimenezi zili choncho chifukwa choti iyeyo ali ndi vuto.” Amakhulupiriranso kuti zinthu “sizingasinthe, kapena sizidzasintha.”