Mawu a M'munsi
a Nthawi zambiri chithunzi chachipembedzo chimakhala chizindikiro kapena chinthu choimira winawake chimene anthu a m’chipembedzo chimenecho amalambira. Mwachitsanzo, m’Tchalitchi cha Orthodox Chakummawa, zithunzi zina zimakhala zoimira Kristu, zina zimaimira Utatu, “oyera mtima,” angelo, kapena, monga m’chitsanzo chili pamwambachi, Mariya amayi a Yesu. Anthu ambiri amalambira zithunzi mofanana ndi mmene anthu ambiri amalambirira mafano amene amagwiritsidwa ntchito popemphera. Zipembedzo zina zimene zimati si zachikristu zili ndi zikhulupiriro zofanana ndi zimenezi ndiponso zimaona chimodzimodzi zithunzi ndi mafano a milungu yawo.