Mawu a M'munsi
b Khalidwe lina limene likutchuka kwambiri masiku ano ndi khalidwe lomwe amuna amadzisamalira ndiponso kudzikongoletsa monyanyira. Zimenezi zachititsa kuti kukhale kovuta kuzindikira amuna amene amagonana ndi amuna anzawo ndi amene satero. Munthu wina anati, mwamuna yemwe ali ndi khalidweli “angakhale wogonana ndi amuna anzake, wabwinobwino, kapena wogonana ndi amuna kapenanso akazi. Koma zimenezi pazokha zilibe kanthu kwa iye, chifukwa choti chikondi chake chimakhala makamaka pa iyeyo basi, choncho kaya amagonana ndi amuna kaya akazi, cholinga chake n’choti adzisangalatse basi.” Ndipo buku lina limati, “Khalidweli latchuka chifukwa choti amuna ogonana ndi amuna anzawo ayamba kuonedwa ngati anthu abwinobwino, komanso chifukwa choti anthu asintha kaonedwe kawo ka mmene mwamuna weniweni ayenera kukhalira.”