Mawu a M'munsi
a Nthenga yomwe akatswiri ofukula za m’mabwinjawo anapeza ndi ya zamoyo zinazake zakale zofanana ndi mbalame. Ndipotu anthu ena amati zamoyo zimenezi n’zimene zikuikira umboni umene wakhala ukusowa wakuti mbalame zinachita kusanduka kuchoka ku nyama zina. Komano akatswiri ambiri asayansi savomereza mfundo imeneyi.