Mawu a M'munsi
a Ndi bwino kusamala mukamagwira mbalame imene yavulala, chifukwa iyoyo siidziwa kuti mukufuna kuithandiza. Komanso pali mbalame zina zimene zimakhala ndi matenda amene angagwirenso anthu. Motero ngati mukufuna kuthandiza mbalame yovulala, ndi bwino kuvala magulovu ndipo muzisamba m’manja mukamaliza. Ngati mukuona kuti mbalameyo ingathe kukuvulazani, musaiyandikire. Mungathenso kuitana akatswiri a zachilengedwe, ngati pangafunike kutero.