Mawu a M'munsi
a Mfundo imeneyi anayambitsa ndi katswiri wina wazachuma wa ku Italy, dzina lake Vilfredo Pareto. Iye ananena kuti nthawi zambiri tingagwire chintchito chachikulu m’kanthawi kochepa. Mfundo imeneyi imagwira ntchito pa zinthu zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, mukamayeretsa m’nyumba, fumbi lambiri limachokera malo amene anthu amakonda kudutsa ndipo malo amenewa amakhala aang’ono kwambiri. Choncho, kungosesa malo amenewo mumakhala kuti mwagwira ntchito yaikulu kuposa kuwononga nthawi kusesa malo akulu omwe sanade kwenikweni.