Mawu a M'munsi
f Katemera wa matenda otupa chiwindi amatha kupangidwa kuchokera ku tizigawo ting’onoting’ono ta magazi. Ngati mukufuna kudziwa zambiri zokhudza tizigawo ting’onoting’ono ta magazi, mungawerenge nkhani yakuti “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” mu Nsanja ya Olonda ya June 15, 2000 komanso ya October 1, 1994. Mfundo zina mungazipeze patsamba 215 m’buku lakuti “Khalanibe M’chikondi cha Mulungu,” lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.