Mawu a M'munsi
b Baibulo limaphunzitsa kuti munthu akafa amangokhala ngati wagona, ndipo amangoyembekezera kuti adzaukitsidwe. (Mlaliki 9:5; Yohane 11:11-14; Machitidwe 24:15) Koma zimene anthu amakhulupirira kuti munthu amakhala ndi chinachake chomwe sichifa munthuyo akamwalira n’zosamveka chifukwa ngati pali chinachake chomwe sichifa, ndiye kuti palibe chifukwa choti akufa adzaukitsidwe.