Mawu a M'munsi
a Munthu wodwala ali ndi ufulu wosankha chithandizo cha chipatala chimene akufuna. Mâmayiko ambiri mumakhala malamulo amene amaonetsetsa kuti ufulu umenewu ukutsatiridwa. Onetsetsani kuti mapepala amene wodwala analembapo zokhudza thandizo la chipatala limene amafuna, ndi olembedwa bwino. Mapepalawo ayeneranso kukhala oti alembedwa chaposachedwapa.