Mawu a M'munsi
a M’madera ena madokotala amalimbikitsa anthu amene ali ndi vuto lodana ndi zakudya zinazake kuti aziyenda ndi mankhwala enaake oti azitha kudzibaya mwamsanga vutoli likayambika. M’madera enanso madokotala amanena kuti ana amene ali ndi vutoli angachite bwino kuvala chibangiri kapena chizindikiro china chomwe chingathandize aphunzitsi awo kudziwa kuti ali ndi vutoli.