Mawu a M'munsi
a Liwu Lachigiriki lomasuliridwa kuti “anadzuma mumzimu” likuchokera ku mneni wakuti (em·bri·maʹo·mai) amene amatanthauza kukhudzidwa mtima kopweteka, kapena kwakukulu. Katswiri wina wa Baibulo akunena kuti: “Panopa lingangotanthauza kuti chisoni chachikulu chinagwira Yesu kotero kuti kudzuma kunangotuluka kokha mumtima Wake.” Liwu lotembenuzidwa kuti ‘kuvutika mwini’ likuchokera ku liwu Lachigiriki (ta·rasʹso) limene limasonyeza kuvutika mtima. Malinga ndi kunena kwa wolemba dikishonale, limatanthauza “kuchititsa munthu kusautsika mumtima, . . . kukhudzidwa ndi kupwetekedwa kapena chisoni chachikulu.” Liwu lakuti “analira” limachokera ku mneni Wachigiriki (da·kryʹo) amene amatanthauza “kugwetsa misoni, kulira mwakachetechete.”