Mawu a M'munsi a Ponena za Yobu, Yehova anati: “Padziko lapansi palibe wina wofanana naye.” (Yobu 1:8) Ndiye kuti Yobu anakhalako Yosefe atamwalira kale komanso Mose asanasankhidwe kukhala mtsogoleri wa Aisiraeli. Choncho zinali zolondola pa nthawiyo kunena kuti panalibe yemwe anali wokhulupirika ngati Yobu.