Mawu a M'munsi
d Kuwonongedwa kwa Babulo ndi chitsanzo chimodzi cha maulosi a m’Baibulo amene anakwaniritsidwa. Koma palinso zitsanzo zina monga za kuwonongedwa kwa mzinda wa Turo ndi Nineve. (Ezekieli 26:1-5; Zefaniya 2:13-15) Komanso ulosi wa Danieli unaneneratu kuti maulamuliro amphamvu a Mediya ndi Perisiya ndiponso Girisi ndi amene adzalamulire pambuyo pa ulamuliro wa Babulo. (Danieli 8:5-7, 20-22) Palinso maulosi ena ambiri onena za Mesiya omwe anakwaniritsidwa pa Yesu Khristu ndipo kuti mumve zambiri za maulosi amenewa, onani Zakumapeto tsamba 199-201.