Mawu a M'munsi
a Pa nthawi ina mneneri Elisa anapereka malangizo ofanana ndi amenewa kwa Gehazi. Pamene ankatumiza mtumiki wakeyu kunyumba ya mayi wina amene mwana wake anamwalira, Elisa anamuuza kuti: “Ukakumana ndi munthu aliyense panjira usam’patse moni.” (2 Mafumu 4:29) Zimene anam’tumazo zinali zofunika kwambiri, choncho sanafunike kutaya nthawi.