Mawu a M'munsi
c Mabaibulo ena amamasulira lembali m’njira yosonyeza kuti munthu angalandire chilango ngati amene wafa ndi mayi yekha. Komabe, olemba mabuku otanthauzira mawu a m’Baibulo amanena kuti mmene mawuwa analembedwera m’Chiheberi, “zikusonyezeratu kuti sankanena za imfa ya mayi yokha.” Onaninso kuti Baibulo silinena kuti chilango cha Yehova chimenechi chinkaperekedwa potengera kukula kwa mwana wosabadwayo.