Mawu a M'munsi
b Patapita zaka zingapo, mtumwi Paulo analemba kalata yopita kwa Aheberi ndipo anasonyeza kuti pangano latsopano limaposa pangano lakale. M’kalatayo, iye anafotokoza momveka bwino kuti pangano latsopano linathetsa pangano lakale. Paulo anapereka mfundo zogwira mtima zimene Akhristu a Chiyuda akanagwiritsa ntchito poyankha Ayuda anzawo omwe ankaumirira Chilamulo cha Mose. Komanso mfundo zamphamvu zimene iye anafotokozazo ziyenera kuti zinalimbitsa chikhulupiriro cha Akhristu ena amene poyamba ankaumirirabe Chilamulo cha Mose.—Aheb. 8:7-13.