Mawu a M'munsi
e Mu 49 C.E., pamene atumwi ndi akulu ankakambirana ngati m’pofunika kuti anthu a mitundu ina azitsatira Chilamulo cha Mose kapena ayi, panali “okhulupirira ena, amene kale anali m’gulu lampatuko la Afarisi.” (Mac. 15:5) Zikuoneka kuti okhulupirira amenewo ankadziwikabe kuti anali Afarisi chifukwa poyamba asanakhale Akhristu anali Afarisi.