Mawu a M'munsi
a Buku lina lokhudza sayansi limafotokoza zimenezi m’njira ina. Limanena kuti kukulungiza zingwe zonsezi m’njira yoti zikwane munyukiliyasi ya selo kungafanane ndi kutenga ulusi wautali makilomita 40 n’kuuika m’kampira kosewerera tenesi, koma n’kuchita zimenezi mwaluso kwambiri moti mbali iliyonse ya ulusiwu ingapezeke mosavuta.—Molecular Biology of the Cell.