Mawu a M'munsi
a Kodi tikudziwa bwanji kuti Atate anaphunzitsa Mwana mmene angalalikirire? Taganizirani izi: Pophunzitsa, Yesu ankagwiritsa ntchito kwambiri mafanizo ndipo zimenezi zinakwaniritsa ulosi umene unalembedwa zaka zambirimbiri asanabadwe. (Sal. 78:2; Mat. 13:34, 35) Apa n’zoonekeratu kuti amene ananena ulosi umenewu, yemwe ndi Yehova, anadziwiratu kuti Mwana wake azidzaphunzitsa anthu pogwiritsa ntchito mafanizo kapena miyambi.—2 Tim. 3:16, 17.