Mawu a M'munsi
c Zikuoneka kuti Mateyu anafotokoza mayeserowa potsatira ndondomeko ya mmene anachitikira, koma Luka analemba Uthenga Wabwino potsatira ndondomeko yosiyana ndi imeneyi. Tikutero chifukwa cha zifukwa zitatu zotsatirazi: (1) Pofotokoza mayesero achiwiri, Mateyu anayamba ndi mawu akuti “kenako,” kusonyeza kuti anali atafotokoza kale mayesero ena. (2) N’zomveka kunena kuti mayesero awiri osaonekerawo, amene akuyamba ndi mawu akuti, “Ngati ndinu mwana wa Mulungu,” akutsatana ndi mayesero oonekeratu ofuna kumuchititsa kuti aphwanye lamulo loyamba. (Eks. 20:2, 3) (3) Komanso n’zomveka kunena kuti mawu a Yesu akuti “Choka Satana!” anawanena pambuyo pa mayesero achitatu komanso omaliza.—Mat. 4:5, 10, 11.