Mawu a M'munsi
a Zikuoneka kuti Abele anabadwa patangopita nthawi yochepa Adamu ndi Hava atathamangitsidwa m’munda wa Edeni. (Gen. 4:1, 2) Lemba la Genesis 4:25 limanena kuti Mulungu anapereka Seti “mʼmalo mwa Abele.” Adamu anali ndi zaka 130 pamene anabereka Seti, pambuyo poti Abele waphedwa mwankhanza. (Gen. 5:3) Choncho Abele ayenera kuti anali ndi zaka 100 pamene Kaini anamupha.