Mawu a M'munsi
a Zimene Ezekieli anafotokoza zokhudza angelo amenewa zimatikumbutsa za dzina la Mulungu lakuti Yehova, limene limatanthauza kuti “Amachititsa Kukhala.” Monga mmene mbali ina ya tanthauzo la dzinali ikusonyezera, Yehova angachititse zinthu zimene analenga kukhala chilichonse chimene chikufunika kuti akwaniritse cholinga chake.—Onani Zakumapeto A4 mu Baibulo la Dziko Latsopano.