Mawu a M'munsi
b Pogwiritsa ntchito mawu akuti “nsanje” Yehova anasonyeza kuti amaona kuti nkhani yokhala okhulupirika kwa iye ndi yaikulu. Zikutipangitsa kuganiza za mkwiyo umene mwamuna amakhala nawo chifukwa cha nsanje mkazi wake akachita zinthu zosakhulupirika. (Miy. 6:34) Mofanana ndi mwamuna ameneyu, Yehova anakwiyiranso anthu amene anachita nawo pangano atayamba kulambira mafano. Buku lina linanena kuti: “Mulungu amachita nsanje . . . chifukwa choti ndi woyera. Popeza kuti iye yekha ndi Woyera . . . , Safuna kuti wina aliyense azipikisana naye.”—Eks. 34:14.