Mawu a M'munsi
a N’zomveka kunena kuti Ezekieli anachita zizindikiro zonsezi anthu akuonerera. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa chakuti pamene anamuuza kuti achite zinthu zina ngati kuphika chakudya komanso kunyamula katundu, Yehova analamula Ezekieli kuti achite zinthu zimenezi “iwo akuona.”—Ezek. 4:12; 12:7.