Mawu a M'munsi
d Baibulo limanenanso kuti “Asuri” wa masiku ano adzaukira anthu a Mulungu n’cholinga chowawonongeratu. (Mika 5:5) Baibulo linaneneratu kuti anthu a Mulungu adzaukiridwa maulendo 4. Linanena kuti adzaukiridwa ndi Gogi wa ku Magogi, mfumu yakumpoto, mafumu a dziko lonse lapansi komanso Asuri. Pamenepa akunena za kuukiridwa kumodzi kumene kwatchulidwa ndi mayina osiyanasiyana.