Mawu a M'munsi
a Yerekezerani njira ziŵiri zimene Paulo anachitira pankhani ya mdulidwe. Ngakhale kuti anadziŵa kuti “mdulidwe ulibe kanthu,” anamdula mnzake woyenda naye Timoteo, amene anali Myuda kumbali ya amake. (1 Akorinto 7:19; Machitidwe 16:3) M’nkhani ya Tito, mtumwi Paulo anapeŵa kumdula chifukwa cholimbana ndi Ayuda. (Agalatiya 2:3) Tito anali Mgiriki ndipo chotero, mosiyana ndi Timoteo, analibe chifukwa chenicheni chodulidwira. Ngati iye, Wamitundu, akanati adulidwe, ‘Kristu sakanapindula naye kanthu.’—Agalatiya 5:2-4.