Mawu a M'munsi
f M’fanizo la nkhosa ndi mbuzi, Mwana wa munthu akufika muulemerero wake panthaŵi ya chisautso chachikulu nakhala pansi kuti apereke chiweruzo. Akuweruza anthu pamaziko akuti kaya anachirikiza abale a Kristu odzozedwa kapena ayi. Maziko oweruzirapo anthu ameneŵa angakhale opanda pake zitakhala kuti podzafika nthaŵi yachiweruzoyo, abale onse a Kristu adzakhala kuti anachokapo kalekale padziko lapansi.—Mateyu 25:31-46.