Mawu a M'munsi
a C. T. Russell atamwalira, buku lomwe linanenedwa kuti ndi voliyumu yachisanu ndi chiŵiri ya Studies in the Scriptures linalembedwa pofuna kuyesa kulongosola mabuku a Ezekieli ndi Chivumbulutso. Mfundo zina za m’bukulo zinazikidwa pa ndemanga za Russell zokhudza mabuku amenewo a m’Baibulo. Komabe, nthaŵi yovumbula tanthauzo la maulosi amenewo inali isanafike, ndipo kuyankhula mwachisawawa, mafotokozedwe operekedwa m’voliyumu imeneyo ya Studies in the Scriptures anali a chimbuuzi. M’zaka zotsatira, chisomo cha Yehova ndi zochitika padziko lapansi zapangitsa Akristu kuzindikira bwino lomwe tanthauzo la mabuku amaulosi amenewo.