Mawu a M'munsi
b N’zoona kuti pali kusiyana pakati pa chiphuphu ndi chiwongola dzanja. Pamene kuli kwakuti chiphuphu chimaperekedwa pofuna kupondereza zinthu kuchitika mwa chilungamo kapena pa zolinga zina za kusaona mtima, chiwongola dzanja chimaperekedwa posonyeza kuyamikira ntchito yabwino yomwe wina wagwira. Zimenezi zalongosoledwa bwino pa “Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga” mu Nsanja ya Olonda yachingelezi ya October 1, 1986.