Mawu a M'munsi
a Popeza kuti Rubeni anali mwana woyamba wa Yakobo, mbadwa zake zomwe zinagwirizana ndi Kora m’chipanduko chakecho ziyenera kuti zinali kuipidwa chifukwa chakuti Mose—mbadwa ya Levi—ndiye amene anali ndi ulamuliro wa utsogoleri pa iwo.