Mawu a M'munsi
a Polalikira Ufumu wa Mulungu, Mboni za Yehova siziloŵerera m’nkhani zandale kapena kupanga magulu oukira boma ngakhale m’mayiko omwe amaziletsa kapena kuzizunza. (Tito 3:1) M’malo mwake, zimayesetsa mosaloŵetsapo ndale kuthandiza mwauzimu monga momwe Yesu ndi ophunzira ake anachitira. Mboni zimayesetsa kuthandiza anthu oona mtima m’madera osiyanasiyana omwe zimakhala kuti aphunzire makhalidwe abwino a m’Baibulo monga chikondi cha pa banja, kuona mtima, kudzisunga, ndiponso makhalidwe abwino a ku ntchito. Kwenikweni, Mboni zimayesetsa kuphunzitsa anthu mmene angatsatirire mfundo zachikhalidwe za m’Baibulo ndiponso kuti aziyembekezera Ufumu wa Mulungu wokha kuti ndiwo udzathetse mavuto a anthu.