Mawu a M'munsi
a Mitengoyo sanali kuisolola m’mphete zija ngakhale pamene Likasalo linali pa malo ake m’chihema. Pachifukwa chimenechi, mitengoyo sanali kuigwiritsa ntchito ina. Komanso Likasalo sanayenera kuligwira. Akanakhala kuti mitengoyo anali kuisolola bwenzi pa ulendo uliwonse akuligwira poloŵetsa mitengoyo m’mphete za likasalo. Zomwe Numeri 4:6 amanena zokhudza “kupisako mphiko zake,” [“kuloŵetsanso mitengo,” NW] kungatanthauze kusendeza mitengoyo pokonzekera kunyamula likasa lolemeralo kupita nalo ku malo atsopano.