Mawu a M'munsi
a Pothirira ndemanga zimene Paulo ananena kuti “chikondi chikhala chilezere, chili chokoma mtima,” Gordon D. Fee yemwe ndi wa maphunziro apamwamba a Baibulo analemba kuti: “Malinga ndi zimene Paulo anaphunzitsa, mawu ameneŵa [kuleza mtima ndi kukoma mtima] akuimira mbali ziŵiri za maganizo a Mulungu kwa anthu (yerekezerani ndi Aroma 2:4). Kulolera kwachikondi kwa Mulungu kukuonekera m’kuletsa kwake ukali pa kupanduka kwa anthu ndiponso kukoma mtima kwake kumene kumaonekera m’nthaŵi zambirimbiri zimene wasonyeza chifundo. Motero Paulo analongosola za chikondi mwa kuyamba kufotokoza mbali ziŵiri zimenezi za Mulungu amene kudzera mwa Kristu analolera ndi kuwachitira chifundo anthu amene anayenera kuwalanga.”