Mawu a M'munsi
b Yehova amanyansidwa ndi zinthu zoipa. Mwachitsanzo, Aefeso 4:29 amafotokoza kuti kalankhulidwe konyansa ndiyo ‘nkhani yovunda.’ Liwu la Chigiriki limene analimasulira kuti “yovunda” kwenikweni limanena za chipatso, nsomba, kapena nyama yoti yawola ndipo ikununkha. Liwu limeneli likusonyeza bwino mmene tiyenera kunyansidwira ndi kalankhulidwe kotukwana kapena kolaula. Mofananamo, Malemba nthaŵi zambiri amanena kuti mafano ali ngati “manyi.” (Deuteronomo 29:17, NW; Ezekieli 6:9, NW) Kuipidwa kwathu ndi manyi kwachibadwa, kukutithandiza kumvetsa mmene Mulungu amaipidwira ndi mafano alionse.