Mawu a M'munsi
b Anzake a Kora achiwembu, Datani ndi Abiramu, anali a fuko la Rubeni. Choncho, mwachionekere iwo sanali kufuna ntchito ya unsembe. M’malo mwake iwo anali kuipidwa ndi utsogoleri wa Mose ndiponso kuti mpaka pa nthaŵi imeneyo, anali asanaloŵebe m’Dziko Lolonjezedwa limene anali kuliyembekezera.—Numeri 16:12-14.