Mawu a M'munsi
c M’nthaŵi za makolo akale, mwamuna aliyense anali kuimira mkazi wake ndi ana ake kwa Mulungu, ngakhalenso kupereka nsembe m’malo mwawo. (Genesis 8:20; 46:1; Yobu 1:5) Komabe, atakhazikitsa Chilamulo, Yehova anaika amuna a m’banja la Aroni kukhala ansembe kuti nsembe ziziperekedwa kudzera mwa iwo. Anthu oukira 250 amenewo mwachionekere sanafune kutsatira kusintha kwa zinthu kumeneku.