Mawu a M'munsi
b Chifukwa chopambana nkhondo zikuluzikulu ndi kutenganso dera limene linali m’manja mwa adani ndiponso zopereka zimene ankatolera chifukwa cha kupambanako, Yerobiamu wachiŵiri ayenera kuti anathandiza kwambiri ufumu wa kumpoto kukhala wachuma.—2 Samueli 8:6; 2 Mafumu 14:23-28; 2 Mbiri 8:3, 4; Amosi 6:2.