Mawu a M'munsi
a M’kalata imene analemba pa November 20, 1861, yopita komwe amapanga ndalama zachitsulo ku United States, Nduna ya Zachuma a Salmon P. Chase anati: “Kuti dziko likhale lamphamvu liyenera kudalira mphamvu za Mulungu, ndipo lingakhale lotetezeka ngati Iye aliteteza. Anthu athu amakhulupirira Mulungu ndipo tiyenera kusonyeza zimenezi pa ndalama zachitsulo za dziko lathu.” Chifukwa cha zimenezi, mu 1864 anayamba kulemba mawu akuti “Timakhulupirira Mulungu” pa ndalama zachitsulo za ku United States.