Mawu a M'munsi
a Zimene zinachitika m’ma 1960 zinali chiyambi chabe cha chizunzo ndi kuphedwa mwankhanza kumene Mboni za m’Malawi zinafunika kupirira kwa zaka pafupifupi makumi atatu. Kuti mumve nkhani yonse, onani bulosha lakuti Mboni za Yehova m’Malaŵi—Nkhani ya Kukhulupirika Kwawo, kapena 1999 Yearbook of Jehovah’s Witnesses, masamba 171 mpaka 212.