Mawu a M'munsi
b Pa chibowo cha Rano Raraku chimene chinkatuluka chiphalaphala pali ziboliboli zambiri. Mpikisano wa anthu ofuna kulamulira pachilumbachi unkayambira pa Rano Kau. Anali kuchita mpikisano wotsika pamalo okwera kwambiri, kusambira kupita pa zilumba zina zazing’ono, kukatenga dzira la mbalame ina yopezeka kumeneko, n’kusambiranso kubwerera pachilumba chija, n’kukweranso pamalo okwera kwambiri aja dzira lili losasweka.