Mawu a M'munsi
a M’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino, Barnaba yemwe anali Mlevi anagulitsa malo ake ndi kupereka ndalama zake kuti zithandize otsatira a Kristu okhala ku Yerusalemu omwe ankafunika chithandizo. Mwina maloŵa anali ku Palestina kapena ku Kupro. Kapenanso mwina anali malo omwe ankafuna kuti adzakhale manda ake omwe Barnaba anagula mu Yerusalemu.—Machitidwe 4:34-37.