Mawu a M'munsi
b Panthaŵi ina Paulo ndi Akristu ena anayi anapita kukachisi kukadziyeretsa mwamwambo. Nthaŵiyi n’kuti Chilamulo chitatha ntchito, komabe Paulo anachita izi potsatira malangizo a amuna akulu a ku Yerusalemu. (Machitidwe 21:23-25) Koma n’kutheka kuti Akristu ena anaganiza kuti iwo sakanaloŵa m’kachisi kapena kuchita mwambo umenewo. Panthaŵiyo anthu anali ndi chikumbumtima chosiyanasiyana, ndipo ndi mmenenso zilili masiku ano.