Mawu a M'munsi
c Buku la Encyclopaedia Judaica limalongosola malamulo “ovuta ndiponso atsatanetsane” ofunika kutsatira kuti nyama ikhale yoyenera kudya mogwirizana ndi miyambo ya Ayuda. Limatchula mphindi zimene nyama iyenera kukhala m’madzi, mmene angaiumikire pa choyanikapo, mtundu wa mchere womwe angaipake, ndiponso maulendo amene angaitsuke m’madzi ozizira.