Mawu a M'munsi
a Zinthu zisanasinthe mu October 1917, dziko la Russia linkagwiritsa ntchito kalendala ya Julius, koma mayiko ambiri anali kugwiritsa ntchito kalendala ya Gregory. M’chaka cha 1917, kalendala ya Julius inkatsalira ndi masiku 13 pa kalendala ya Gregory. Zinthu zitasintha, akuluakulu a dzikolo anayamba kugwiritsa ntchito kalendala ya Gregory, ndipo apa dziko la Russia linayamba kugwiritsa ntchito kalendala yofanana ndi imene mayiko ena onse anali kugwiritsa ntchito. Koma Tchalitchi cha Orthodox chinapitiriza kugwiritsa ntchito kalendala ya Julius chifukwa cha zikondwerero zake, n’kumaitcha kuti kalendala yachikale. Mungathe kumva anthu ku Russia akunena za kukondwerera Khirisimasi pa January 7. Komabe, musaiwale kuti pa kalendala ya Gregory, January 7 ndi December 25 pa kalendala ya Julius. Motero, anthu ambiri ku Russia amakhala ndi zikondwerero izi panyengo ya tchuthiyi: December 25, Khirisimasi ya kumayiko a kumadzulo kwa Ulaya; January 1, tsiku lopanda zochitika zachipembedzo la Chaka Chatsopano; January 7, Khirisimasi ya a Orthodox; January 14, Chaka Chatsopano pa kalendala yachikale.