Mawu a M'munsi
a Anthu amenewa anathandiza kwambiri pamaphunziro a zinenero zimene anthu olemba Baibulo anagwiritsira ntchito. Mu 1506, Reuchlin anafalitsa buku lake la malamulo a chinenero cha Chiheberi. Bukuli linathandiza kuti anthu aphunzire mozama Malemba Achiheberi. Mu 1516, Erasmus anafalitsa Baibulo la Malemba Achigiriki Achikristu popanda kusintha chinenerocho.